Acts 26:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atachokapo adauzana kuti, “Munthuyu sakuchita chilichonse choyenera kumuphera kapena kumponyera m'ndende.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo atapita padera analankhula wina ndi mnzake, nanena, Munthu uyu sanachita kanthu koyenera imfa, kapena nsinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inatuluka mʼchipindamo, ndipo pamene imayankhula inati, “Munthu uyu sanachite kanthu koyenera kuphedwa kapena kumangidwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo atapita padera analankhula wina ndi mnzace, nanena, Munthu uyu sanacita kanthu koyenera imfa, kapena nsinga.