Acts 26:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ayuda onse akudziŵa za moyo wanga wonse kuyambira ndili mwana. Akudziŵa m'mene ndinkakhalira chiyambire pakati pa anthu a mtundu wanga, ndiponso ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mayendedwe a moyo wanga tsono, kuyambira pa chibwana changa, amene anakhala chiyambire mwa mtundu wanga m'Yerusalemu, awadziwa Ayuda onse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ayuda onse akudziwa za moyo wanga mmene ndakhalira kuyambira ndili mwana, kuchokera pachiyambi cha moyo wanga mʼdziko lathu ndiponso mu Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mayendedwe a moyo wanga tsono, kuyambira pa cibwana canga, amene anakhala ciyambire mwa mtundu wanga m'Yerusalemu, awadziwa Ayuda onse;