Acts 26:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo adandidziŵa kuyambira kale, ndipo ngati afuna, angathe kundichitira umboni kuti moyo wanga wonse ndakhala Mfarisi, mmodzi wa gulu lija limene limasamala chipembedzo chathu koposa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
andidziwa ine chiyambire, ngati afuna kuchitapo umboni, kuti ndinakhala Mfarisi monga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa chipembedzero chathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo akundidziwa kuyambira kalekale ndipo angathe kuchitira umboni kuti ndakhala ndili Mfarisi moyo wanga wonse, mmodzi wa gulu limene limasamala chipembedzo chathu koposa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
andidziwa ine ciyambire, ngati afuna kucitapo umboni, kuti ndinakhala Mfarisi monga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa cipembedzero cathu.