Acts 26:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafuko onse khumi ndi aŵiri a mtundu wathu, popembedza Mulungu usana ndi usiku mosafookera, amayembekeza kudzalandira zimene Iye adalonjezazo. Mwakuti nchifukwa cha chiyembekezo chimenechi, amfumu, kuti Ayuda akundineneza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kufikira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Chifukwa cha chiyembekezo ichi, Mfumu, andinenera Ayuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ili ndi lonjezo limene mafuko athu khumi ndi awiri akuyembekezera kuti likwaniritsidwe pamene akupembedza Mulungu molimbika usana ndi usiku. Wolemekezeka Mfumu, nʼchifukwa cha chiyembekezo chimenechi Ayuda kuti akundiyimba mlandu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kunkira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Cifukwa ca ciyembekezo ici, Mfumu, andinenera Ayuda.