Acts 27:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono popeza kuti dooko silinali labwino kukhalako pa nthaŵi yachisanu, ambiri mwa iwo adafuna kuchokako, nayesa kuti angathe kukafika ku Fenikisi nkukakhala kumeneko pa nthaŵi yachisanu. Fenikisi linali dooko la ku Krete, loloza kumwera chakumadzulo, ndiponso kumpoto chakumadzulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popeza dooko silinakoma kugonapo nyengo yachisanu, unyinji unachita uphungu ndi kuti amasule nachokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Fenikisi, ndi kugonako, ndilo dooko la ku Krete, loloza kumpoto ndi kumwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza kuti dookolo silinali labwino kukhalako nthawi yozizira anthu ambiri anaganiza kuti tichoke. Ife tinkayembekeza kukafika ku Foinikisi ndi kukhala kumeneko nthawi yachisanu. Ili linali dooko la ku Krete, limene limaloza kummwera cha kumadzulo ndiponso kumpoto cha kumadzulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popezadooko silinakoma kugonapo nyengo yacisanu, unyinji unacita uphungu ndi kutiamasule nacokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Foinika, ndi kugonako, ndilo dooko la ku Krete, loloza kumpoto ndi kumwela.