Acts 27:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mphepo yakumwera itayamba kuwomba monyengerera, anthu aja adayesa kuti tsopano apeza mpata woti achite zimene ankafuna. Motero adanyamuka ulendo, nayenda m'mbali mwa chilumba chija cha Krete.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo poomba pang'ono mwera, poyesa kuti anaona chofunirako, anakoka nangula, napita m'mbali mwa Krete.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mphepo yochokera kummwera itayamba kuwomba pangʼonopangʼono, anthuwo anaganiza kuti apeza chimene amafuna; kotero analowetsa nangula ndipo anayamba kuyenda mʼmbali mwa chilumba cha Krete.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo poomba pang'ono mwela, poyesa kuti anaona cofunirako, anakoka nangula, napita m'mbali mwa Krete.