Acts 27:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tidakwera chombo chochokera ku Adramitio chimene chinali chokonzeka kale kupita ku madooko a ku Asiya, ndipo tidanyamuka. Aristariko, Mmasedoni wa ku mzinda wa Tesalonika, anali nafe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene tidalowa m'ngalawa ya ku Adramitio ikati ipite kunka ku malo a ku mbali ya Asiya, tinakankha, ndipo Aristariko Mmasedoniya wa ku Tesalonika, anali nafe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tinakwera sitima ya pamadzi yochokera ku Adramutiyo imene inali yokonzeka kale kupita ku madooko a ku Asiya, ndipo tinanyamuka. Aristariko, wa ku Makedoniya wa ku mzinda wa Tesalonika, anali nafe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene tidalowam'ngalawa ya ku Adramutiyo ikati ipite kunka ku malo a ku mbali ya Asiya, dnakankha, ndipo Aristarko Mmakedoniya wa ku Tesalonika, anali nafe.