Acts 27:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi yaitali anthu aja sadadye kanthu. Tsono Paulo adaimirira pakati pao nati, “Abale, mukadamvera zija ndidaanena inezi, osachoka ku Krete, sibwenzi zinthu zitawonongeka nkutayika chotere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene atakhala nthawi yaikulu osadya kanthu, Paulo anaimirira pakati pao, nati, Amuna inu, mukadamvera ine, osachoka ku Krete, osadzitengera kuonongeka ndi kutayika kumene.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu aja atakhala nthawi yayitali osadya, Paulo anayimirira pakati pawo ndipo anati, “Anthu inu, mukanamvera malangizo anga oti tisachoke ku Krete: zonsezi sizikanawonongeka ndi kutayika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene atakhala nthawi yaikuru osadya kanthu, Paulo anaimirira pakati pao, nati, Amuna inu, mukadamvera ine, osacoka ku Krete, osadzitengera kuonongeka ndi kutayika kumene.