Acts 27:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuli pafupi kucha, Paulo adaŵapempha onse aja kuti adyeko kanthu. Adaŵauza kuti, “Mwakhala masiku khumi ndi anai tsopano mitima ili m'malere, nthaŵi yonseyi osadya kapena kulaŵa kanthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popeza kulinkucha, Paulo anawachenjeza onse adye kanthu, nati, Lero ndilo tsiku lakhumi ndi chinai limene munalindira, ndi kusala chakudya, osalawa kanthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kutatsala pangʼono kucha, Paulo anawawumiriza anthu onse kuti adye. Iye anati, “Kwa masiku khumi ndi anayi mwakhala mukuda nkhawa ndipo simumadya kanthu kalikonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popeza kulinkuca, Paulo anawacenjeza onse adye kanthu, nati, Lero ndilo tsiku lakhumi ndi cinai limene munalindira, ndi kusala cakudya, osalawa kanthu.