Acts 27:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kutacha, anthu sadazindikire mtundawo, koma adaona bondo la nyanja lamchenga. Tsono adaganiza kuti ngati nkotheka, akakocheze chombo kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kutacha sanazindikira dzikolo; koma anaona pali bondo la mchenga; kumeneko anafuna, ngati nkutheka, kuyendetsako ngalawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kutacha, anthu sanazindikire dzikolo, koma anaona pomwe sitima zimayimapo pamodzi ndi mchenga wa pa gombe. Iwo anaganiza zokocheza sitimayo kumeneko ngati zikanatheka kutero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kutaca sanazindikira dzikolo; koma anaona pali bondo la mcenga; kumeneko anafuna, ngati nkutheka, kuyendetsako ngalawa.