Acts 27:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma chombo chija chidakatsakamira pa mchenga wobisika ndi madzi, ndipo chidaima. Mbali yakutsogolo ya chombocho idajima, kotero kuti sichidathe kuyendanso. Ndipo mbali yakumbuyo idaonongeka ndi mphamvu ya mafunde.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pofika pamalo pokomana mafunde awiri, anatsamitsapo ngalawa; ndipo kulikulu kunatsama, ndi kukhala kosasunthika, koma kumakaliro kunasweka ndi mphamvu ya mafunde.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma sitimayo inagunda mchenga wobisika ndipo inayima. Mbali ya kutsogolo ya sitimayo inakanirira ndipo sinathe kuyendanso, ndipo mbali yakumbuyo inasweka ndi kuwomba kwa mafunde.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pofika pamalo pokomana mafunde awiri, anatsamitsapo ngalawa; ndipo kulikuru kunatsama, ndi kukhala kosasunthika, koma kumakaliro kunasweka ndi mphamvu ya mafunde.