Acts 27:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mtsogoleri wa asilikali uja adafuna kupulumutsa Paulo, motero adaŵaletsa. Adalamula kuti onse otha kusambira, adziponye m'madzi, asambire kuti akafike ku mtunda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, anawaletsa angachite cha uphungu wao; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziponya m'nyanja, nafike pamtunda,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma wolamulira asilikali uja anafuna kupulumutsa Paulo ndipo anawaletsa kuchita zimene anakonza. Iye analamulira asilikali kuti amene amatha kusambira kuti adziponye mʼmadzi ndi kuyamba kukafika pa mtunda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, anawaletsa angacite ca uphungu wao; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziporiya m'nyanja, nafike pamtunda,