Acts 27:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tidayenda pang'onopang'ono pa masiku angapo, nkukafika pafupi ndi Kinido movutikira. Tsono popeza kuti mphepo idaativuta zedi, tidalephera kupitirira ulendo wathu molunjika, choncho tidadzera kumwera kwa chilumba cha Krete, titabzola Salimone.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene tidapita pang'onopang'ono masiku ambiri, ndi kufika movutika pandunji pa Kinido, ndipo popeza siinatilolanso mphepo, tinapita m'tseri mwa Krete, pandunji pa Salimone;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tinayenda pangʼonopangʼono kwa masiku ambiri ndipo tinakafika kufupi ndi Knido movutikira. Pamene mphepo sinatilole kupitirira ulendo wathu molunjika, tinadzera kummwera kwa chilumba cha Krete, moyangʼanana ndi Salimoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene tidapita pang'ono pang'ono masiku ambiri, ndi kufika mobvutika pandunji pa Knido, ndipo popeza siinatilolanso mphepo, tinai pita m'tseri mwa Krete, pandunji pa Salimone;