Acts 28:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale akumeneko atamva za ife, adabwera mpaka ku Bwalo la Apio ndiponso ku Nyumba za Alendo Zitatu kudzatichingamira. Paulo ataona ataŵaona, adayamika Mulungu, nalimba mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuchokera kumeneko abalewo, pakumva za ife, anadza kukomana nafe ku Bwalo la Apio, ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu; ndipo pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale kumeneko atamva kuti tikubwera, anabwera kudzakumana nafe mpaka ku bwalo la Apiyo ndiponso ku nyumba za alendo zitatu. Atawaona anthu amenewa Paulo anayamika Mulungu ndipo analimbikitsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kucokera kumeneko abalewo, pakumva za ife, anadza kukomana nafe ku Bwalo la Apiyo, ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu; ndipo pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima.