Acts 28:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patapita masiku atatu, Paulo adasonkhanitsa atsogoleri a Ayuda akomweko. Atasonkhana, iye adaŵauza kuti, “Abale anga, ine ndili kuno ngati mkaidi wochokera ku Yerusalemu. Ngakhale sindidalikwire mtundu wathu, kapena miyambo ya makolo athu, komabe ndidaperekedwa kwa Aroma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, atapita masiku atatu, anaitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, ananena nao, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindinachita kanthu kakuipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, anandipereka wam'nsinga kuchokera ku Yerusalemu ku manja a Aroma;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patapita masiku atatu, Paulo anasonkhanitsa pamodzi atsogoleri a Ayuda. Atasonkhana, Paulo anawawuza kuti, “Abale anga, ngakhale kuti ine sindinachite kanthu kalikonse kulakwira mtundu wathu kapena miyambo ya makolo athu, koma anandigwira mu Yerusalemu ndi kundipereka mʼmanja mwa Aroma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, atapita masiku atatu, anaitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, ananena nao, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindinacita kanthu kakuipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, anandipereka wam'nsinga kucokera ku Yerusalemu ku manja a Aroma;