Acts 28:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu apamenepo adatichitira zabwino kwambiri. Adatilandira bwino natisonkhera moto, chifukwa kudaayamba kugwa mvula ndipo kunkazizira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akunja anatichitira zokoma zosachitika pena ponsepo; pakuti anasonkha moto, natilandira ife tonse, chifukwa cha mvula inalinkugwa, ndi chifukwa cha chisanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a pa chilumbacho anatichitira zokoma zimene sizichitika kawirikawiri. Iwo anakoleza moto natilandira tonse chifukwa kumagwa mvula ndipo kumazizira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akunja anaticitira zokoma zosacitika pena ponsepo; pakuti anasonkha moto, natilandira ife tonse, cifukwa ca mvula inalinkugwa, ndi cifukwa ca cisanu.