Acts 28:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleriwo adamuyankha kuti, “Ife sitidalandirepo makalata ochokera ku Yudeya onena za inu. Palibenso wina mwa abale athu amene adafika kuno kudzatifotokozera kapena kudzatiwuza zoipa za inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iye, Ife sitinalandira akalata onena za inu ochokera ku Yudeya, kapena sanadza kuno wina wa abale ndi kutiuza kapena kulankhula kanthu koipa ka inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anayankha kuti, “Ife sitinalandire kalata iliyonse yochokera ku Yudeya yonena za iwe, ndipo palibe mmodzi wa abale amene anachokera kumeneko anafotokoza kapena kunena kalikonse koyipa ka iwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iye, Ife sitinalandira akalata onena za inu ocokera ku Yudeya, kapena sanadza kuno wina wa abale ndi kutiuza kapena kulankhula kanthu koipa ka inu.