Acts 28:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono popeza kuti anthuwo sadamvane, adangochokapo. Komabe asanachoke, Paulo adaawonjezapo mau amodzi aŵa akuti, “Mzimu Woyera adaanena zoona pamene adaauza makolo anu mwa mneneri Yesaya kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma popeza sanavomerezana, anachoka atanena Paulo mau amodzi, kuti, Mzimu Woyera analankhula kokoma mwa Yesaya Mneneri kwa makolo anu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anayamba kuchoka popeza sanagwirizane pakati pawo Paulo atanena mawu awa omaliza akuti, “Mzimu Woyera anayankhula zoona za makolo anu pamene Iye ananena kudzera mwa Mneneri Yesaya kuti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma popeza sanabvomerezana, anacoka atanena Paulo mau amodzi, kuti, Mzimu Woyera analankhula kokoma mwa Yesaya Mneneri kwa makolo anu,