Acts 28:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithu mtima wa anthu a mtundu uwu wauma, agonthetsa makutu ao ndipo atseka maso ao, kuwopa kuti angaone ndi maso ao, ndipo angamve ndi makutu ao, angamvetse ndi mtima wao, natembenukira mwa Ine kuti ndiŵachitiritse.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti mtima wa anthu awa watupatu, ndipo m'makutu mwao mmolema kumva, ndipo maso ao anawatseka; kuti angaone ndi maso, nangamve ndi makutu, nangazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo Ine ndingawachiritse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti mtima wa anthu ndi wokanika; mʼmakutu mwawo ndi mogontha, ndipo atsinzina kuti asaone kanthu. Mwina angapenye ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka, Ineyo nʼkuwachiritsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mtima wa anthu awa watupatu, Ndipo m'makutu mwao mmolemakumva, Ndipo masoao anawatseka; Kuti angaone ndi maso, Nangamve ndi makutu, Nangazindikire ndi mtima, Nangatembenuke, Ndipo Ine ndingawaciritse.