Acts 28:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu aja ankayembekeza kuti thupi lake litupa, kapena kuti agwa mwadzidzidzi nkufa. Adakhala akumuyang'ana nthaŵi yaitali, koma ataona kuti palibe chilichonse chachilendo chimene chamchitikira, adasintha maganizo nati, “Ameneyu ndi mmodzi wa milungu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anayesa kuti adzatupa, kapena mwini wake kugwa kufa pomwepo; koma m'mene adalindira nthawitu, naona kuti sikunampweteka, anapindula, nati, Ndiye Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu anayembekezera kuti thupi lake litupa kapena agwa ndi kufa mwadzidzidzi, koma anadikira nthawi yayitali. Ataona kuti palibe kanthu kachilendo kanamuchitikira anasintha maganizo awo nanena kuti iye ndi mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anayesa kuti adzatupa, kapena mwini wace kugwa kufa pomwepo; koma m'mene adalindira nthawitu, naona kuti sikunampweteka, anapindula, nati, Ndiye Mulungu.