Acts 28:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bambo wake wa Publioyo anali gone, chifukwa ankadwala malungo ndi kamwazi. Paulo adaloŵa m'chipinda chake nayamba kupemphera, ndipo adamsanjika manja nkumuchiritsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunatero kuti atate wake wa Publioyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, namchiritsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abambo ake anali gone, chifukwa amadwala malungo ndi kamwazi. Paulo analowa mʼchipinda chake kukawaona, ndipo atapemphera, anasanjika manja ake pa iwo nawachiritsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunatero kuti atate wace wa Popliyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, namciritsa.