Acts 3:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamzindikira kuti ndi yemwe uja amene ankakhala pa Khomo Lokongola la Nyumba ya Mulungu. Ndipo adazizwa ndithu ndi kudabwa ndi zimene zidamchitikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
namzindikira iye, kuti ndiye amene anakhala pa Khomo Lokongola la Kachisi: ndipo anadzazidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa pa ichi chidamgwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
anamuzindikira kuti ndi yemwe uja ankakhala pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola, ndipo anazizwa ndi kudabwa ndi zimene zinamuchitikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
namzindikira iye, kuti ndiye amene anakhala pa Khomo Lokongola la Kacisi: ndipo anadzazidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa pa ici cidamgwera.