Acts 3:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu uja adaakangamira Petro ndi Yohane, ndipo anthu onse adadabwa, naŵathamangira ku Khonde lotchedwa Khonde la Solomoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma m'mene anagwira Petro ndi Yohane, anawathamangira pamodzi anthu onse kukhonde lotchedwa la Solomoni, alikudabwa ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wopempha uja akuyenda pamodzi ndi Petro ndi Yohane, anthu onse anadabwa ndipo anawathamangira iwo kumalo wotchedwa Khonde la Solomoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma m'mene anagwira Petro ndi Yohane, anawathamangira pamodzi anthu onse ku khumbi lochedwa la Solomo, alikudabwa ndithu.