Acts 3:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Petro adaona zimenezi, adalankhula nawo anthuwo, adati, “Inu Aisraele, bwanji mukuzizwa ndi zimenezi? Bwanji mukutiyang'ana ngati kuti tamuyendetsa munthuyu ndi mphamvu zathuzathu? Kodi mukuyesa kuti nchifukwa choti ndife opembedza Mulungu kopambana?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma m'mene Petro anachiona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israele, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi chipembedzo chathu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Petro ataona zimenezi anawawuza kuti, “Inu Aisraeli, chifukwa chiyani mukudabwa ndi zimene zachitikazi? Bwanji mukuyangʼana ife ngati kuti tamuyendetsa munthuyu ndi mphamvu yathu kapena chifukwa cha kupembedza kwathu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma m'mene Petro anaciona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israyeli, muzizwa naye bwanji ameneyo? kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi cipembedzo cathu?