Acts 3:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyai, koma Mulungu wa makolo athu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, adapereka ulemerero kwa Yesu, Mtumiki wake. Inu mudampereka kwa adani ake ndi kumkana pamaso pa Pilato, pamene Pilatoyo adaatsimikiza kuti ammasula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wake Yesu; amene inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, wamulemekeza mtumiki wake Yesu. Amene inu munamukana pamaso pa Pilato ndi kumupereka Iye kuti aphedwe, ngakhale kuti Pilato anafuna kuti amumasule.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu wa Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wace Yesu; amene, inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.