Acts 3:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena adaanyamula munthu wina wopunduka miyendo chibadwire. Masiku onse ankamuika pa khomo la Nyumba ya Mulungu lotchedwa “Khomo Lokongola,” kuti iye azipempha kwa anthu oloŵa m'Nyumbamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu wina wopunduka miyendo chibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kachisi lotchedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa m'Kachisi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo munthu wolumala chibadwire ankanyamulidwa tsiku ndi tsiku kukayikidwa pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola kuti azikapempha amene amalowa ku bwalo la Nyumbayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu wina wopunduka miyendo cibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kacisi lochedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa m'Kacisi;