Acts 3:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja Mose adati, ‘Ambuye Mulungu adzasankhula mmodzi pakati pa abale anu, kuti akhale Mneneri wanu monga ine. Mudzamvere zonse zimene Iye adzakuuzeni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mosetu anati, Mbuye Mulungu adzaukitsira inu mneneri mwa abale anu, ngati ine; mudzamvera iye m'zinthu zilizonse akalankhule nanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Mose anati, ‘Ambuye Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri monga ine kuchokera pakati pa anthu anu; mumvere zonse zimene iye akuwuzeni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mosetu anati, Mbuye Mulungu adzaukitsira inu mneneri mwa abale anu, ngati ine; mudzamvera iye m'zinthu ziri zonse akalankhule nanu.