Acts 4:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Petro ndi Yohane akulankhulabe ndi anthu aja, kudadza ansembe ena pamodzi ndi mkulu wa asilikali a ku Nyumba ya Mulungu, ndi Asaduki.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma m'mene analikulankhula ndi anthu, ansembe ndi mdindo wa ku Kachisi ndi Asaduki anadzako,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Petro ndi Yohane amayankhula ndi anthu, kunabwera ansembe, mkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndiponso Asaduki.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma m'mene analikulankhula ndi anthu, ansembe ndi mdindo wa kuKacisi ndi Asaduki anadzako,