Acts 4:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kuwopa kuti mbiriyi ingaŵande ponseponse, tiyeni tiwachenjeze moopseza kuti polankhula ndi munthu aliyense asatchulenso dzina la Yesu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komatu tiwaopse asalankhulenso m'dzina ili kwa munthu aliyense, kuti chisabukenso kwa anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma kuti mbiriyi isapitirire kuwanda pakati pa anthu, ife tiwachenjeze anthu amenewa kuti asayankhulenso kwa wina aliyense mʼdzina la Yesu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komatu tiwaopse asalankhulenso m'dzina ili kwa munthu ali yense, kuti cisabukenso kwa anthu.