Acts 4:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abwalowo adaŵachenjezanso moopseza koposa kale, naŵamasula. Sadapeze njira yoti nkuŵalangira, popeza kuti anthu onse ankatamanda Mulungu chifukwa cha zimene zidaachitikazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atawonjeza kuwaopseza anawamasula. Sanathe kugwirizana njira yowalangira, chifukwa anthu onse amayamika Mulungu chifukwa cha zimene zinachitika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, cifukwa ca anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu cifukwa ca comwe cidacitika.