Acts 4:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene iwo adamva zimenezi, onse adayamba kupemphera ndi mtima umodzi. Adati, “Ambuye, ndinu amene mudalenga dziko lakumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi zonse zili m'menemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene adamva, anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse zili m'menemo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu atamva zimenezi anafuwula ndi mtima umodzi napemphera kwa Mulungu. Iwo anati, “Ambuye wolamulira zonse, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndiponso zonse zili mʼmenemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene adamva, anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse ziri m'menemo;