Acts 4:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa Mzimu Woyera mudalankhulitsa kholo lathu Davide, mtumiki wanu, pamene adati, “ ‘Chifukwa chiyani anthu akunja adakalipa, anthu a mitundu ina adaganiziranji zopandapake?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene mwa Mzimu Woyera, pakamwa pa kholo lathu Davide mtumiki wanu, mudati, Amitundu anasokosera chifukwa chiyani? Nalingirira zopanda pake anthu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu munayankhula mwa Mzimu Woyera kudzera pakamwa pa Davide kholo lathu, mtumiki wanu kuti, “ ‘Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu, ndipo akonzekera kuchita zopandapake?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene mwa Mzimu Woyera, pakamwa pa kholo lathu Davine mtumiki wanu, mudati, Amitundu anasokosera cifukwaciani? Nalingirira zopanda pace anthu?