Acts 4:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafumu a dziko lapansi adakonzekera, akulu a Boma adasonkhana pamodzi kulimbana ndi Chauta, ndiponso ndi wodzozedwa wake uja?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anadzindandalitsa mafumu a dziko, ndipo oweruza anasonkhanidwa pamodzi, kutsutsana ndi Ambuye, ndi Khristu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo; ndipo olamulira asonkhana pamodzi kulimbana ndi Ambuye ndi wodzozedwa wakeyo.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anadzindandalitsa mafumu a dziko, Ndipo oweruza anasonkhanidwa pamodzi, Kutsutsana ndi Ambuye, ndi Kristu wace.