Acts 4:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Gulu lonse la okhulupirira linali la mtima umodzi, ndi la maganizo amodzi. Panalibe munthu amene ankati, “Zimene ndiri nazo nzangazanga,” koma aliyense ankapereka zake zonse kuti zikhale za onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo unyinji wa iwo akukhulupirira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananena mmodzi kuti kanthu ka chuma anali nacho ndi kake ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Okhulupirira onse anali a mtima umodzi, ndi maganizo amodzi. Palibe munthu amene amati zomwe anali nazo zinali zake zokha, koma amagawana chilichonse chimene anali nacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo unyinji wa iwo akukhulupira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananena mmodzi kuti kanthu ka cuma anali naco ndi kace ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana.