Acts 5:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo adagwa pansi ku mapazi a Petro, naafa. Pamene achinyamata aja adaloŵa, adampeza atafa kale. Adamnyamula nakamuika pafupi ndi mwamuna wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anagwa pansi pomwepo pa mapazi ake, namwalira; ndipo analowa anyamatawo, nampeza iye wafa, ndipo anamnyamula kutuluka naye, namuika kwa mwamuna wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomweyo anagwa pansi pa mapazi a Petro ndipo anamwalira. Ndipo anyamata aja analowa, napeza kuti wafa kale, anamunyamula ndi kukamuyika pafupi ndi mwamuna wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anagwa pansi pomwepo pa mapazi ace, namwalira; ndipo analowa anyamatawo, nampeza iye wafa, ndipo anamnyamula kuturuka naye, namuika kwa mwamuna wace.