Acts 5:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atumwi ankachita zizindikiro ndi zozizwitsa zambiri pakati pa anthu. Onse okhulupirira Khristu ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Khonde la Solomoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zinachitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khonde la Solomoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atumwi anachita zizindikiro zodabwitsa ndi zozizwitsa zambiri pakati pa anthu. Ndipo onse okhulupirira ankasonkhana pamodzi mu Khonde la Solomoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwa manja aatumwi zizindikilo ndi zozizwa zambiri zinacitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khumbi la Solomo.