Acts 5:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu ankatulutsira odwala ao m'miseu yamumzinda, nkumaŵagoneka pa mabedi ndi pa mphasa, kuti Petro podutsapo, chithunzithunzi chake chokha ena mwa iwo chiŵafike.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kotero kuti ananyamulanso natuluka nao odwala kumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale chithunzi chake chigwere wina wa iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha zimenezi, anthu anabweretsa odwala mʼmisewu ya mu mzinda nawagoneka pa mabedi ndi pa mphasa kuti chithunzi chokha cha Petro chikhudze ena mwa iwo iye akamadutsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kotero kuti ananyamulanso naturuka nao odwala Ifumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale cithunzi cace cigwere wina wa iwo.