Acts 5:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunkasonkhananso anthu ochuluka ochokera ku midzi yozungulira Yerusalemu. Anali atanyamula anthu odwala, ndiponso ena osautsidwa ndi mizimu yoŵaipitsa. Onsewo ankachiritsidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ochokera kumidzi yozungulira Yerusalemu, alikutenga odwala, ndi ovutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anachiritsidwa onsewa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ochuluka ochokera ku mizinda yayingʼono ozungulira Yerusalemu amasonkhananso atatenga odwala awo ndi iwo amene amasautsidwa ndi mizimu yoyipa ndipo onsewo amachiritsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ocokera ku midzi yozungulira Yerusalemu, alikutenga odwala, ndi obvutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anaciritsidwa onsewa.