Acts 5:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atumwi aja adamveradi zimenezi, adakaloŵa m'Nyumba ya Mulungu m'mamaŵa, nayamba kuphunzitsa. Pamene mkulu wa ansembe onse adafika pamodzi ndi anzake aja, adaitanitsa msonkhano wa Bungwe Lalikulu, ndiye kuti Bwalo lonse la akuluakulu a Aisraele. Tsono adatuma anthu kuti apite ku ndende akaŵatenge atumwi aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atamva ichi, analowa m'Kachisi mbandakucha, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene anali naye, nasonkhanitsa a bwalo la akulu, ndi akulu onse a ana a Israele, natuma kundende atengedwe ajawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kutacha mmawa, atumwi analowa mʼbwalo la mʼNyumba ya Mulungu, monga anawuzidwa ndipo anayamba kuphunzitsa anthu. Mkulu wa ansembe pamodzi ndi omuthandiza ake amene anali naye anafika, anayitanitsa msonkhano wa Bwalo Lalikulu, ndilo bwalo la akulu onse a Israeli. Anatuma alonda kuti akatenge atumwi aja kundende.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atamva ici, analowa m'Kacisi mbanda kuca, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene analinaye, nasonkhanitsa a bwalo la akuru, ndi akulu onse a ana a Israyeli, natuma kundende atengedwe ajawo.