Acts 5:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma munthu wina adadzaŵauza kuti, “Anthu amene mudaŵatsekera m'ndende aja, ali m'Nyumba ya Mulungu ndipo akuphunzitsa anthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza wina nawafotokozera, kuti, Taonani, amuna aja mudawaika m'ndende ali m'Kachisi, alikuimirira ndi kuphunzitsa anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo wina anabwera ndi kuti, “Taonani! Anthu aja amene munawatsekera mʼndende ali ku Nyumba ya Mulungu ndipo akuphunzitsa anthu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza wina nawafotokozera, kuti, Taonani, amuna aja mudawaika m'ndende ali m'Kacisi, alikuimirira ndi kuphunzitsa anthu.