Acts 5:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adati, “Paja tidakuletsani mwamphamvu kuti musaphunzitse konse m'dzina la Yesu, koma inu mwafalitsa zophunzitsa zanuzo m'Yerusalemu monse, ndipo mukufuna kusenzetsa ife imfa ya munthu ameneyu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Ife tinakuletsani kuti musaphunzitsenso mʼdzina ili, koma inu mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mukufuna kutisenzetsa imfa ya munthu ameneyu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nanena, Tidakulamulirani cilamulire, musaphunzitsa kuchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi ciphunzitso canu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.