Acts 5:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Petro adamufunsa kuti, “Iwe Ananiya, chifukwa chiyani walola mtima wako kugwidwa ndi Satana mpaka kumanamiza Mzimu Woyera pakupatula ndalama zina za munda wako?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Petro anati, Ananiya, Satana anadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Petro anamufunsa kuti, “Hananiya, chifukwa chiyani Satana anadzaza chotere mu mtima wako kuti unamize Mzimu Woyera ndipo wapatula ndi kusunga ndalama?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Petro anati, Hananiya, Satana anadzaza mtima wako cifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wace wa mundawo?