Acts 5:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma wina mwa iwo, Mfarisi dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa Malamulo, amene anthu onse ankamlemekeza, adaimirira. Adalamula kuti anthu aja abaapita panja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ananyamukapo wina pa bwalo la akulu, ndiye Mfarisi, dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa chilamulo, wochitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang'ono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Mfarisi wina dzina lake Gamalieli, mphunzitsi wa malamulo, amene anthu onse amamulemekeza, anayimirira ndi kulamula kuti atumwiwo ayambe apita panja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ananyamukapo wina pa bwalo la akuru, ndiye Mfarisi, dzina lace Gamaliyeli, mphunzitsi wa cilamulo, wocitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang'ono.