Acts 5:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu si kale pamene munthu wina dzina lake Teudasi adaabwera nkuyesa kudzimveketsa, ndipo anthu ngati mazana anai adamtsata. Iye uja adaphedwa, ndipo anthu onse amene ankamtsata aja adabalalikana natheratu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti asanafike masiku ano anauka Teudasi, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu anaphatikana naye, chiwerengero chao ngati mazana anai; ndiye anaphedwa; ndi onse amene anamvera iye anamwazika, napita pachabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti masiku a mʼmbuyomu kunali Teuda amene anadzitchukitsa, ndipo anthu pafupifupi 400 anamutsatira. Iye anaphedwa ndipo omutsatira akewo anabalalitsidwa, zonse zinatheratu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti asanafike masiku ana anauka Teuda, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu anaphatikana naye, ciwerengero cao ngati mazana anai; ndiye anaphedwa; ndi onse amene anamvera iye anamwazika, napita pacabe.