Acts 5:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake, pa nthaŵi ya kalembera, padabweranso wina dzina lake Yudasi, wa ku Galileya, nakopa anthu ambiri kuti amtsate. Iyenso adaphedwa, ndipo anthu onse amene ankamtsata aja adabalalikana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atapita ameneyo, anauka Yudasi wa ku Galileya, masiku a kulembedwa, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake, nthawi ya kalembera kunalinso Yudasi wa ku Galileya, ndipo anatsogolera gulu la anthu amene anawukira, iyenso anaphedwa ndipo anthu ake onse anabalalitsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atapita ameneyo, anauka Yuda wa ku Galileya, masiku a kulembedwa, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.