Acts 5:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usanaugulitse, sunali wako kodi? Ndipo utaugulitsa, suja ndalama zake zinali m'manja mwako? Nanga udalola bwanji zoterezi mumtima mwako? Pamenepatu sudanamize anthu, koma wanamiza Mulungu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene unali nao, sunali wako kodi? Ndipo pamene unagulitsa sunali m'manja mwako kodi? Bwanji chinalowa ichi mumtima mwako? Sunanyenga anthu, komatu Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi sunali wako usanagulitse? Ndipo utagulitsa ndalamazo sizinali mʼmanja mwako kodi? Nʼchiyani chinakuchititsa zimenezi? Iwe sunanamize anthu koma Mulungu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene unali nao, sunali wako kodi? ndipo pamene unaugulitsa sunali m'manja mwako kodi? bwanji cinalowa ici mumtima mwako? sunanyenga anthu, komatu Mulungu.