Acts 5:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Petro adamufunsa kuti, “Bwanji mudapangana kuyesa Mzimu wa Ambuye? Ndipotu anthu amene akaika mwamuna wanu ndi aŵa ali pakhomoŵa, akunyamulani inunso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kutuluka nawe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Petro anati kwa iye, “Bwanji inu munapangana kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona! Anthu amene anakayika mwamuna wako mʼmanda ali pa khomo, ndipo adzakunyamula iwenso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kuturuka nawe.