Acts 6:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku amenewo ophunzira aja ankachulukirachulukira. Koma Ayuda olankhula Chigriki anali ndi dandaulo pa Ayuda olankhula Chiyuda kuti akazi ao amasiye sankasamalidwa bwino pamene zachifundo za tsiku ndi tsiku zinkagaŵidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma masiku awo, pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmasiku amenewo pamene chiwerengero cha ophunzira chinkachuluka, Ayuda a Chihelene pakati pawo anadandaula chifukwa cha Ayuda a Chihebri chifukwa amasiye awo samawagawira chakudya cha tsiku ndi tsiku.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma masiku awo, pakucurukitsa ophunzira, kunauka cidandaulo, Aheleniste kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa citumikiro ca tsiku ndi tsiku.