Acts 6:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero adautsa mitima ya anthu, ya akuluakulu ao, ndiponso ya aphunzitsi a Malamulo. Iwoŵa adamuukira Stefano, namgwira, nkupita naye ku Bungwe Lalikulu la Ayuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anautsa anthu, ndi akulu, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye kubwalo la akulu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero anawutsa mitima ya anthu, akulu ndi aphunzitsi amalamulo. Anamugwira Stefano ndi kumubweretsa ku Bwalo Lalikulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anautsa anthu, ndi akuru, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye ku bwalo la akulu,