Acts 6:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kudabwera anthu ena a ku Kirene ndi a ku Aleksandriya, a ku nyumba yamapemphero yotchedwa “Nyumba Yamapemphero ya Opatsidwa Ufulu.” Iwoŵa pamodzi ndi ena a ku Silisiya ndi a ku Asiya adayamba kutsutsana ndi Stefano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anauka ena a iwo ochokera m'sunagoge wa Alibertino, ndi Akirene, ndi Aaleksandriya, ndi mwa iwo a ku Silisiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panauka mtsutso kuchokera kwa anthu a ku Kurene ndi a ku Alekisandriya komanso a ku dera la Silisiya ndi Asiya, otchedwa a Sunagoge ya Mfulu. Anthu amenewa anayamba kutsutsana ndi Stefano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anauka ena a iwo ocokera m'sunagoge wa Alibertino, ndi Akurenayo, ndi Aalesandreyo, ndi mwa iwo a ku Kilikiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano.